Liwu Lanu ndalimva
Koma ngat Yona
Mtimawu uli ndi mantha
Kodi amva?
Ndithawire kuti?
Kulira Kwa anawa nakumva
Ndi maso anga nawawona
Akufunitsitsa kuthawa Ku eguputo
Mose napemphera
Tioloka bwanji nyanjayi?
Angamve zawamisala
Ngakhale ataona nkhondo?
Ngat kotheka njirayi indipitire
Loreni nditenge inayi
Mtimawu wazizwa, pa mphambano njo!
Ndilowere kuti?
Thukuta kamu kamu napemphera
Ngat nkotheka chikhochi chindidutse
Komabe funa Kwanu kuchitidwe
This poem has not been translated into any other language yet.
I would like to translate this poem