Gwire Tambala pakhosi
Kaione ndithu sitimayo
Bongololo wanji uyu?
Khaleni Phee!
Ankaganizanji oyikonza
Ngwautali mtunda
Mponde mponde
mpikasano wazidendende
Tikamuone ndithu bongolo
Nakwawa pa njanji yakwathu
Dzuwa likuyasamula tifika ndithu
Khaleni kudikilira bongololo ayende
Kuchibwano nakandira, ngati mlenje
Mpitawu udodometsa
Anaukonza atawona wambewa?
This poem has not been translated into any other language yet.
I would like to translate this poem