Bwerako kumene uliko
Makone ndakusowa
Phwaa! Mtima nusweka
Kalata ya mayi kuiwerenga
Ndiwauzanji mayi
Msozi ufuna kusefukira
Ngati shire munyengo ya mvula
Mtimawu ufuna kulira
Kuiwerenga kalata ya mayi malawi
Mwanaga kudziko kuno udza liti?
Ndikumbuka bwino Mayi wanga
Kamachita manyado
Analidi mayiwa. Pamtima pawo
Ndipo panali mphala yanga
Ooh! mayi wanga Malawi
Ndilire bwanji mwanawanune
Mtimawu ngosweka
Kaona pakhomo po
Anawa akanali kulira
Ndibwerera bwanji kunyumbako
Kudziko kuno ndine mfulu
chikhalidwe changa si tchimo
Nkhungu langa n'lachilendo
Tsitsi langa lokwirimbinyika
Nyani wamudzimu
Wokondedwa mayi
Kalata yanu naiwerenga
Pamtima pa mayi afrika
Ndikhumba kudzagona pamenepo
Phukusi langa ndamanga
Ulendo wokaona mayi
Mayi wanga Malawi
This poem has not been translated into any other language yet.
I would like to translate this poem