Mtimawu wadzadza ndi chikondi
Ngati napolo ufuna kuphulika
Tanditsepure patsayapa
Ndimpsopsono wako wadzetsa tsembwe
Udekhetse mtimawu, ulinda iwe
Ngati kanjere ka mpiru,
Ndilore ndifese chikondichi mumtima mwako
Nuchitengulira ngati mbande
Chikule monga m'bawa
Zidzulu tubvi pamthuzi pake nasewera
Iwe ndine tsitsi litabwira ufa
Pambalipo nawonera
Mtimawu ndi ng'anjo yamoto
Malawi ofukira ndi chikondi
Ndimpsopsono wako wodzetsa tsembwe
Udekhetse mtimawu, ulinda iwe
This poem has not been translated into any other language yet.
I would like to translate this poem