Mphepo Yakwathu Poem by Chikondi Daniel Dziko

Mphepo Yakwathu

Kaomba Kamphepo ka kwathu
Dzuwa likuwala
Ana akusewera masanje
Wina nakhala mayi wina bambo
A fisi nalira dzuwa lalowa
Awa anali masewero a moyo

Kamphepo ka kwathu
Kodza kamvula katawaza
Fumbi litazilala, kadza mwa zii!
Dongo lathu titakowa
Naumba galimoto
Ena naumba za mawaya ena za njerwa
Awa anali maloto athu

Nyau! Nyau!
Kadza ndi mfuwu kamphepo kakwathu
Zonse Nataya liwiro Kobo!
chipako nda amakaka
Akapoli nda kamano tithamangitsana
Wasilamba patsogolo chilembwe napita
Awa anali magule akwathu

COMMENTS OF THE POEM
READ THIS POEM IN OTHER LANGUAGES
Close
Error Success